Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 35:10-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Nenandi ana a Israyeli, nuti nao, Pakuoloka inu Yordano kulowa m'dziko la Kanani,

11. muikire midzi ikukhalireni midzi yopulumukirako; kuti wakupha mnzace wosati dala athawireko.

12. Ndipo midziyo ikukhalireni yakupulumuka wolipsa; kuti wakupha mnzace asafe, kufikira ataima pamaso pa msonkhano amweruze.

13. Ndipo midziyo muipereke ikukhalireni midzi isanu ndi umodzi yopulumukirako.

14. Mupereke midzi itatu tsidya lino la Yordano, ndi midzi itatu mupereke m'dziko la Kanani, ndiyo yopulumukirako.

15. Midzi isanu ndi umodzi imene ndiyo yopulumukirako ana a Israyeli, ndi mlendo, ndi wokhala pakati pao; kuti ali yense adamupha munthu osati dala athawireko.

Werengani mutu wathunthu Numeri 35