1. Ndipo Yehova ananena ndi Mose m'zidikha za Moabu, pa Yordano, ku Yeriko, ndi kuti,
2. Uza ana a Israyeli, kuti apatseko Alevi colowa cao cao, midzi yokhalamo; muwapatsenso Alevi mabusa akuzungulira midzi.
3. Ndipo midzi ndiyo yokhalamo iwowa; ndi mabusa akhale a ng'ombe zao, ndi zoweta zao, inde nyama zao zonse.
4. Ndipo mabusa a midziyo, imene muipereke kwa Alevi ndiwo a mikono cikwi cimodzi kuyambira kulinga kufikira kunja.