Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 33:7-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Ndipo anacokera ku Etamu, nayenda nabwerera ku Pihahiroti, ndiko kutsogolo kwace kwa Baala Zefoni; namanga iwo patsogolo pa Migidoli.

8. Ndipo anacokera ku Pihahiroti, naoloka pakati pa nyanja nalowa m'cipululu; nayenda ulendo wa masiku atatu m'cipululu ca Etamu, namanga m'Mara.

9. Ndipo anacokera ku Mara, nayenda nafika ku Elimu, ku Elimu ndiko kuli akasupe khumi ndi awiri a madzi, ndi akanjedza makumi asanu ndi awiri; namanga iwo komweko.

10. Ndipo anacokera ku Elimu, nayenda namanga ku Nyanja Yofiira.

11. Nacokera ku Nyanja Yofiira, nayenda namanga m'cipululu ca Sini.

12. Nacokera ku cipululu ca Sini, nayenda namanga m'Dofika.

13. Nacokera ku Dofika, nayenda namanga m'Alusi.

14. Nacokera ku Alusi, nayenda namanga m'Refidimu; kumeneko kunalibe madzi kuti anthu amwe.

15. Ndipo anacokera ku Refidimu, nayenda namanga m'cipululu ca Sinai.

16. Nacokera ku cipululu ca Sinai, nayenda namanga m'Kibiroti Hatava.

17. Nacokera ku Kibiroti Hatava, nayenda namanga m'Hazeroti.

18. Nacokera ku Hazeroti, nayenda namanga m'Ritima.

19. Nacokera ku Ritima, nayenda namanga m'Rimoni Perezi.

20. Nacokera ku Rimoni Perezi, nayenda namanga m'Libina.

21. Nacokera ku Libina, nayenda namanga m'Risa.

22. Nacokera ku Risa, nayenda namanga m'Kehelata.

23. Nacokera ku Kehelata, nayenda namanga m'phiri la Saferi.

24. Nacokera ku phiri la Saferi, nayenda namanga n'Harada.

25. Nacokera ku Harada, nayenda namanga m'Makeloti.

26. Nacokera ku Makeloti, nayenda namanga m'Tahata.

Werengani mutu wathunthu Numeri 33