Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 33:10-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Ndipo anacokera ku Elimu, nayenda namanga ku Nyanja Yofiira.

11. Nacokera ku Nyanja Yofiira, nayenda namanga m'cipululu ca Sini.

12. Nacokera ku cipululu ca Sini, nayenda namanga m'Dofika.

13. Nacokera ku Dofika, nayenda namanga m'Alusi.

14. Nacokera ku Alusi, nayenda namanga m'Refidimu; kumeneko kunalibe madzi kuti anthu amwe.

15. Ndipo anacokera ku Refidimu, nayenda namanga m'cipululu ca Sinai.

16. Nacokera ku cipululu ca Sinai, nayenda namanga m'Kibiroti Hatava.

17. Nacokera ku Kibiroti Hatava, nayenda namanga m'Hazeroti.

18. Nacokera ku Hazeroti, nayenda namanga m'Ritima.

19. Nacokera ku Ritima, nayenda namanga m'Rimoni Perezi.

20. Nacokera ku Rimoni Perezi, nayenda namanga m'Libina.

Werengani mutu wathunthu Numeri 33