Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 31:38-47 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

38. Ndipo ng'ombe zidafikira zikwi makumi atatu mphambu zisanu ndi cimodzi; pamenepo msonkho wa Yehova ndiwo makumi asanu ndi awiri mphambu ziwiri.

39. Ndipo aburu anafikira zikwi makumi atatu ndi mazana asanu; pamenepo msonkho wa Yehova ndiwo makumi asanu ndi limodzi mphambu mmodzi.

40. Ndipo anthu anafikira zikwi khumi ndi zisanu ndi cimodzi; pamenepo msonkho wa Yehova ndiwo anthu makumi atatu mphambu awiri.

41. Ndipo Mose anapereka zamsonkhozo, ndizo nsembe yokweza ya Yehova, kwa Eleazara wansembe, monga Yehova adamuuza Mose.

42. Ndipo kunena za gawo la ana a Israyeli, limene Mose adalicotsa kwa anthu ocita nkhondowo,

43. (ndipo gawo la khamulo ndilo nkhosa zikwi mazana atatu mphambu makumi atatu kudza zisanu ndi ziwiri mphambu mazana asanu,

44. ndi ng'ombe zikwi makumi atatu mphambu zisanu ndi cimodzi,

45. ndi aburu zikwi makumi atatu ndi mazana asanu,

46. ndi anthu zikwi khumi ndi zisanu ndi cimodzi,)

47. mwa gawolo la ana a Israyeli Mose anatenga munthu mmodzi mwa makumi asanu, ndi zoweta momwemo, nazipereka kwa Alevi, akusunga udikiro wa kacisi wa Yehova; monga Yehova adamuuza Mose.

Werengani mutu wathunthu Numeri 31