Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 31:36-44 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

36. Ndipo limodzi la magawo awiri, ndilo gawo la iwo adaturuka kunkhondo, linafikira nkhosa zikwi mazana atatu mphambu makumi atatu kudza zisanu ndi ziwiri mphambu mazana asanu.

37. Ndi msonkho wa Yehova wankhosa ndiwo mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu ndi awiri mphambu zisanu.

38. Ndipo ng'ombe zidafikira zikwi makumi atatu mphambu zisanu ndi cimodzi; pamenepo msonkho wa Yehova ndiwo makumi asanu ndi awiri mphambu ziwiri.

39. Ndipo aburu anafikira zikwi makumi atatu ndi mazana asanu; pamenepo msonkho wa Yehova ndiwo makumi asanu ndi limodzi mphambu mmodzi.

40. Ndipo anthu anafikira zikwi khumi ndi zisanu ndi cimodzi; pamenepo msonkho wa Yehova ndiwo anthu makumi atatu mphambu awiri.

41. Ndipo Mose anapereka zamsonkhozo, ndizo nsembe yokweza ya Yehova, kwa Eleazara wansembe, monga Yehova adamuuza Mose.

42. Ndipo kunena za gawo la ana a Israyeli, limene Mose adalicotsa kwa anthu ocita nkhondowo,

43. (ndipo gawo la khamulo ndilo nkhosa zikwi mazana atatu mphambu makumi atatu kudza zisanu ndi ziwiri mphambu mazana asanu,

44. ndi ng'ombe zikwi makumi atatu mphambu zisanu ndi cimodzi,

Werengani mutu wathunthu Numeri 31