Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 3:46-51 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

46. Kunena za mazana awiri ndi makumi asanu ndi awiri kudza atatuwo oyamba kubadwa a ana a Israyeli, akuposa Alevi, akaomboledwe,

47. ulandire masekeli asanu pa munthu mmodzi; uwalandire pa muyeso wa sekeli wa malo opatulika (sekeli ndiwo magera makumi awiri);

48. nupereke ndarama zimene akuposawo anaomboledwa nazo kwa Aroni ndi kwa ana ace amuna.

49. Pamenepo Mose analandira ndarama zaom bola nazo kwa iwo akuposa aja adawaombola Alevi;

50. analandira ndaramazo kwa oyamba kubadwa a ana a Israyeli; masekeli cikwi cimodzi mphambu mazana atatu kudza makumi asanu ndi limodzi mphambu asanu, kuyesa sekeli wa malo opatulika.

51. Ndipo Mose anapatsa Aroni ndi ana ace ndarama zaom bola nazo monga mwa mau a Yehova, monga Yehova adauza Mose.

Werengani mutu wathunthu Numeri 3