Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 3:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Mibadwo ya Aroni ndi Mose, tsiku lija Yehova ananena ndi Mose m'phiri la Sinai, ndi iyo.

2. Ndipo maina ao a ana amuna a Aroni ndi awa: Woyamba Nadabu, ndi Abihu, Eleazara, ndi Itamara.

3. Awa ndi maina a ana amuna a Aroni, ansembe odzozedwawo, amene anawadzaza manja ao acite nchito ya nsembe.

4. Koma Nadabu ndi Abihu anafa pamaso pa Yehova muja anabwera nao moto wacilendo pamaso pa Yehova, m'cipululu ca Sinai, ndipo analibe ana; koma Eleazara ndi Itamara anacita Debito ya nsembe pamaso pa atate wao Aroni.

Werengani mutu wathunthu Numeri 3