24. nsembe yace yaufa, ndi nsembe zace zothira za ng'ombe, za nkhosa zamphongo, ndi za ana a nkhosa, monga mwa kuwerenga kwace, ndi kutsata lemba lace;
25. ndi tonde mmodzi akhale nsembe yaucimo; pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, nsembe yace yaufa, ndi nsembe yace yothira.
26. Ndi tsiku lacisanu ng'ombe zisanu ndi zinai, nkhosa zamphongo ziwiri, ana a nkhosa khumi ndi anai, a caka cimodzi, opanda cirema;
27. ndi nsembe yace yaufa, ndi nsembe zace zothira, za ng'ombe, za nkhosa zamphongo, ndi za ana a nkhosa, monga mwa kuwerenga kwace, ndi kutsata lemba lace;
28. ndi tonde mmodzi akhale nsembe yaucimo; pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yace yaufa, ndi nsembe yace yothira.
29. Ndi tsiku lacisanu ndi cimodzi ng'ombe zisanu ndi zitatu, nkhosa zamphongo ziwiri, ana a nkhosa khumi ndi anai, a caka cimodzi, opanda cirema;
30. ndi nsembe yace yaufa, ndi nsembe zace zothira, za ng'ombe, za nkhosa zamphongo, ndi za ana a nkhosa, monga mwa kuwerenga kwace, ndi kutsata lemba lace;
31. ndi tonde mmodzi akhale nsembe yaucimo; pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, nsembe yace yaufa, ndi nsembe yace yothira.
32. Ndi tsiku lacisanu ndi ciwiri ng'ombe zisanu ndi ziwiri, nkhosa zamphongo ziwiri, ana a nkhosa khumi ndi anai, a caka cimodzi, opanda cirema;
33. ndi nsembe yace yaufa, ndi nsembe zace zothira, za ng'ombe, za nkhosa yamphongo, ndi za ana a nkhosa, monga mwa kuwerenga kwace, ndi kutsata lemba lace;
34. ndi tonde mmodzi akhale nsembe yaucimo; pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, nsembe yace yaufa, ndi nsembe yace yothira.
35. Tsiku lacisanu ndi citatu muzikhala nalo tsiku loletsa; musamacita nchito ya masiku ena;