Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 28:21-31 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

21. upereke limodzi la magawo khumi likhale la mwana wa nkhosa mmodzi; uzitero ndi ana a nkhosa asanu ndi awiri;

22. ndi tonde mmodzi akhale nsembe yaucimo, yakutetezera inu.

23. Mupereke izi pamodzi ndi nsembe yopsereza ya m'mawa, ndiyo ya nsembe yopsereza kosalekeza.

24. Momwemo mupereke cakudya ca nsembe yamoto ca pfungo lokoma la Yehova, tsiku ndi tsiku, masiku asanu ndi awiri, cakupereka pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yace yothira.

25. Ndipo tsiku lacisanu ndi ciwiri mukhale nako kusonkhana kopatulika; musamacita nchito ya masiku ena.

26. Momwemonso tsiku la zipatso zoyamba, pobwera nayo nsembe ya ufa watsopano kwa Yehova, m'madyerero anu a masabata, muzikhala nako kusonkhana kopatulika; musamacita nchito ya masiku ena.

27. Pamenepo muzipereka nsembe yopsereza ya pfungo lokoma kwa Yehova; ng'ombe zamphongo ziwiri, nkhosa yamphongo imodzi, ana a nkhosa asanu ndi awiri a caka cimodzi;

28. ndi nsembe yace ya ufa wosalala wosanganiza ndi mafuta, atatu a magawo khumi akhale a ng'ombe imodzi, awiri a magawo khumi akhale a nkhosa yamphongo imodzi,

29. limodzi la magawo khumi likhale la mwana wa nkhosa mmodzi, momwemo ndi ana a nkhosa asanu ndi awiri;

30. tonde mmodzi wakutetezera inu.

31. Mupereke izi pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yace yaufa, zikhale kwa inu zopanda cirema, ndi nsembe zace zothira.

Werengani mutu wathunthu Numeri 28