Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 26:6-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Hezeroni, ndiye kholo la banja la Ahezeroni; Karimi, ndiye kholo la banja la Akarimi.

7. Iwo ndiwo mabanja a Arubeni; owerengedwa ao ndiwo zikwi makumi anai mphambu zitatu kudza mazana asanu ndi awiri mphambu makumi atatu,

8. Mwana wamwamuna wa Palu ndiye Eliyabu.

9. Ndi ana a Eliyabu: Nemueli, ndi Datani ndi Abiramu. Iwo ndiwo Datani ndi Abiramu omwe aja oitanidwa a khamu, amene anatsutsana ndi Mose ndi Aroni mu msonkhano wa Kora, mula anatsutsana ndi Yehova;

10. ndipo dziko linayasama pakamwa pace, ndi kuwameza pamodzi ndi Kora, pakufa msonkhano uja; muja mote unaononga amuna mazana awiri ndi makumi asanu, nakhala iwo cizindikilo.

11. Koma sanafa ana amuna a Kora.

12. Ana amuna a Simeoni monga mwa mabanja ao ndiwo: Nemueli, ndiye kholo la banja la Anemueli; Yamini, ndiye kholo la banja la Ayamini; Yakini, ndiye kholo la banja la Ayakini;

Werengani mutu wathunthu Numeri 26