Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 26:41-57 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

41. Iwo ndiwo ana a Benjamini monga mwa mabanja ao; ndipo owerengedwa ao ndiwo zikwi makumi anai mphambu zisanu kudza mazana asanu ndi limodzi.

42. Mwana wamwamuna wa Dani monga mwa mabanja ace ndiye Suhamu, ndiye kholo la banja la Asuhamu. Iwo ndiwo mabanja a Dani monga mwa mabanja ao.

43. Mabanja aose a Asuhamu monga mwa owerengedwa ao ndiwo zikwi makumi asanu ndi limodzi mphambu zinai kudza mazana anai.

44. Ana amuna a Aseri monga mwa mabanja ao ndiwo: Yimna, ndiye kholo la banja la Ayimna; Yisivi, ndiye kholo la banja la Ayisivi; Beriya, ndiye kholo la banja la Aberiya.

45. Ana a Beriya ndiwo: Heberi, ndiye kholo la banja la Aheberi; Malikiyeli, ndiye kholo la banja la Amalikiyeli.

46. Ndipo dzina la mwana wamkazi wa Aseri ndiye Sera.

47. Iwo ndiwo mabanja a ana amuna a Aseri monga mwa owerengedwa ao, zikwi makumi asanu mphambu zitatu kudza mazana anai.

48. Ana amuna a Nafitali monga mwa mabanja ao ndiwo: Yazeli, ndiye kholo la banja la Ayazeli; Guni, ndiye kholo la banja la Aguni;

49. Yezeri, ndiye kholo la banja la Ayezeri; Silemu, ndiye kholo la banja la Asilemu.

50. Iwo ndiwo mabanja a Nafitali, monga mwa mabanja ao; ndipo owerengedwa ao ndiwo zikwi makumi anai mphambu zisanu kudza mazana anai.

51. Iwo ndiwo owerengedwa ao a ana a Israyeli, zikwi mazana asanu ndi limodzi mphambu cimodzi kudza mazana asanu ndi awiri mphambu makumi atatu.

52. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

53. Dziko ligawikire iwowa monga mwa kuwerenga kwa maina, likhale colowa cao.

54. Ocurukawo, uwacurukitsire colowa cao; ocepawo uwacepetsere colowa cao; ampatse yense colowa cace monga mwa owerengedwa ace.

55. Koma aligawe ndi kucita maere; colowa cao cikhale monga mwa maina a mafuko a makolo ao,

56. Agawire ocuruka ndi ocepa colowa cao monga mwa kucita maere.

57. Ndipo awa ndi owerengedwa ao a Alevi monga mwa mabanja ao: Gerisoni, ndiye kholo la banja la Agerisoni; Kohati, ndiye kholo la banja la Akohati; Merari, ndiye kholo la banja la Amerari.

Werengani mutu wathunthu Numeri 26