Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 26:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo kunali, utatha mliriwo, Yehova ananena ndi Mose ndi Eleazara mwana wa Aroni wansembe, nati,

2. Werenga khamu lonse la ana a Israyeli, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, monga mwa nyumba za makolo ao, onse akuturukira kunkhondo m'Israyeli.

3. Pamenepo Mose ndi Eleazara wansembe ananena nao m'zidikha za Moabu pa Yordano kufupi ku Yeriko, ndi kuti,

4. Awawerenge kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu; monga Yehova anawauza Mose ndi ana a Israyeli, amene adaturuka m'dziko la Aigupto.

5. Rubeni, ndiye woyamba kubadwa wa Israyeli; ana amuna a Rubeni ndiwo: Hanoki, ndiye kholo la banja la Ahanoki; Palu, ndiye kholo la banja la Apalu;

Werengani mutu wathunthu Numeri 26