Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 24:14-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Ndipo tsopano, taonani, ndimuka kwa anthu a mtundu wanga; tiyeni, ndidzakulangizani, ndi kukuuzani zimene anthu awa adzacitira anthu anu, masiku otsiriza.

15. Ndipo ananena fanizo lace, nati,Balamu mwana wa Beori anenetsa,Ndi munthu wotsinzina masoyo anenetsa;

16. Anenetsa wakumva mau a Mulungu,Ndi kudziwa nzeru ya Wam'mwambamwamba,Wakuona masomphenya a Wamphamvuyonse,Wakugwa pansi wopenyuka maso;

17. Ndimuona, koma tsopano ai; Ndimpenya, koma si pafupi ai;Idzaturuka nyenyezi m'Yakobo,Ndi ndodo yacifumu idzauka m'Israyeli,Nidzakantha malire a Moabu,Nidzapasula ana onse a Seti,

18. Ndi Edomu adzakhala ace ace,Seiri lomwe lidzakhala lace lace, ndiwo adani ace;

19. Koma Israyeli adzacita zamphamvu.Ndipo wina woturuka m'Yakobo adzacita ufumu;Nadzapasula otsalira m'mudzi.

20. Ndipo anayang'ana ku Amaleki, nanena fanizo lace, nati,Amaleki ndiye woyamba wa amitundu;Koma citsiriziro cace, adzaonongeka ku nthawi zonse.

21. Ndipo anayang'ana Akeni, nanena fanizo lace, nati,Kwanu nkokhazikika,Wamanga cisa cako m'thanthwe.

22. Koma Kaini adzaonongeka,Kufikira Asuri adzakumanga nsinga.

23. Ndipo ananena fanizo lace, nati,Ha! adzakhala ndi moyo ndani pakucita ici Mulungu?

24. Koma zombo zidzafika kucokera ku doko la Kitimu,Ndipo adzasautsa Asuri, nadzasautsa Ebere,Koma iyenso adzaonongeka.

25. Ndipo Balamu anauka, namuka nabwerera kumalo kwace; ndi Balaki yemwe anamka njira yace.

Werengani mutu wathunthu Numeri 24