Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 24:12-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Ndipo Balamu anati kwa Balaki, Kodi sindinauzanso amithenga anu amene munawatumiza kwa ine, ndi kuti,

13. Cinkana Balaki akandipatsa nyumba yace yodzala ndi siliva ndi golidi, sindikhoza kutumpha mau a Yehova, kucita cokoma kapena coipa ine mwini wace; conena Yehova ndico ndidzanena ine?

14. Ndipo tsopano, taonani, ndimuka kwa anthu a mtundu wanga; tiyeni, ndidzakulangizani, ndi kukuuzani zimene anthu awa adzacitira anthu anu, masiku otsiriza.

15. Ndipo ananena fanizo lace, nati,Balamu mwana wa Beori anenetsa,Ndi munthu wotsinzina masoyo anenetsa;

16. Anenetsa wakumva mau a Mulungu,Ndi kudziwa nzeru ya Wam'mwambamwamba,Wakuona masomphenya a Wamphamvuyonse,Wakugwa pansi wopenyuka maso;

17. Ndimuona, koma tsopano ai; Ndimpenya, koma si pafupi ai;Idzaturuka nyenyezi m'Yakobo,Ndi ndodo yacifumu idzauka m'Israyeli,Nidzakantha malire a Moabu,Nidzapasula ana onse a Seti,

18. Ndi Edomu adzakhala ace ace,Seiri lomwe lidzakhala lace lace, ndiwo adani ace;

19. Koma Israyeli adzacita zamphamvu.Ndipo wina woturuka m'Yakobo adzacita ufumu;Nadzapasula otsalira m'mudzi.

Werengani mutu wathunthu Numeri 24