Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 23:21-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

21. Sayang'anira mphulupulu iri m'Yakobo,Kapena sapenya kupulukira kuli m'lsrayeli.Yehova Mulungu wace ali ndi iye,Ndi mpfuu wa mfumu uli pakati pao,

22. Mulungu awaturutsa m'Aigupto;Mphamvu yace ikunga ya njati.

23. Pakuti palibe nyanga pakati pa Yakobo,Kapena ula mwa Israyeli;Pa nyengo yace adzanena kwa Yakobo ndi Israyeli,Cimene Mulungu acita.

24. Taonani, anthuwo auka ngati mkango waukazi,Nadzitukumula ngati mkango waumuna:Sugonansokufikira utadya nyama yogwira,Utamwa mwazi wa zophedwa.

25. Ndipo Balaki anati kwa Balamu, Usawatemberera konse, kapena kuwadalitsa konse.

26. Koma Balamu anayankha nati kwa Balaki, Sindinakuuzani ndi kuti, Ciri conse acinena Yehova, comweco ndizicita?

27. Ndipo Balaki anati kwa Balamu, Tiyetu, ndimuke nawe kumalo kwina; kapena kudzakomera pamaso pa Mulungu kuti unditembererere iwo pokhala kumeneko.

28. Ndipo Balaki anamka naye Balamu pamwamba pa Peori, popenyana ndi cipululu.

29. Ndipo Balamu anati kwa Balaki, Mundimangire pano maguwa a nsembe asanu ndi awiri, nimundikonzere pano ng'ombe zisanu ndi ziwiri, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri.

30. Ndipo Balaki anacita monga adanena Balamu, napereka ng'ombe ndi nkhosa yamphongo pa guwa la nsembe liri laose.

Werengani mutu wathunthu Numeri 23