Ndipo anthu anadza kwa Mose, nati, Tacimwa, popeza tinanena motsutsana ndi Yehova, ndi inu; pempherani kwa Yehova kuti aticotsere njokazi. Ndipo Mose anawapempherera anthu.