Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 21:12-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Pocokapo anayenda ulendo, namanga mahema m'cigwa ca Zaredi.

13. Atacokako anayenda ulendo, namanga mahema tsidya tina la Arinoni, wokhala m'cipululu, wogwera ku malire a Aamori; popeza Arinoni ndiwo malire a Moabu, pakati pa Moabu ndi Aamori.

14. Cifukwa cace, ananena m'buku la Nkhondo za Yehova,Vahebi m'Sufa,Ndi miyendo ya Arinoni;

15. Ndi zigwa za miyendoyoZakutsikira kwao kwa Ari,Ndi kuyandikizana ndi malire a Moabu.

16. Ndipo atacokapo anamuka ku Been, ndico citsime cimene Yehova anacinena kwa Mose, Sonkhanitsa anthu, ndipo ndidzawapatsa madzi.

17. Pamenepo Israyeli anayimba nyimbo iyi:Tumphuka citsime iwe; mucithirire mang'ombe;

18. Citsime adakumba mafumu,Adacikonza omveka a anthu;Atanena mlamuli, ndi ndodo zao.Ndipo atacoka kucipululu anamuka ku Matana;

19. atacoka ku Matana ku Nahaliyeli; atacoka ku Nahaliyeli ku Bamoti;

20. atacoka ku Bamoti ku cigwa ciri m'dziko la Moabu, ku mutu wa Pisiga, popenyana ndicipululu.

21. Ndipo Israyeli anatuma amithenga kwa Sihoni mfumu ya Aamori, ndi kuti,

Werengani mutu wathunthu Numeri 21