Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 20:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo ana a Israyeli, ndilo khamu lonse, analowa m'cipululu ca Zini mwezi woyamba; ndipo anthu anakhala m'Kadesi; kumeneko anafa Miriamu, naikidwakomweko.

2. Ndipo khamulo linasowa madzi; pamenepo anasonkhana kutsutsana nao Mose ndi Aroni.

3. Ndipo anthu anatsutsana ndi Mose, nanena, nati, Mwenzi titangomwalira muja abale athu anamwalira pamaso pa Yehova!

4. Mwalowa nao bwanji msonkhano wa Yehova m'cipululu muno, kuti tifere mommuno, ife ndi zoweta zathu?

5. Ndipo munatikwezeranji kutiturutsa m'Aigupto, kutilowetsa m'malo oipa ano? Si malo a mbeu awa, kapena mkuyu, kapena mpesa kapena makangaza; ngakhale madzi akumwa palibe.

6. Ndipo Mose ndi Aroni anacoka pamaso pa msonkhano kumka ku khomo la cihema cokomanako, nagwa nkhope zao pansi; ndipo ulemerero wa Yehova unaonekera iwo.

7. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

8. Tenga ndodoyo, nusonkhanitse khamulo; iwe ndi Aroni mbale wako, munene ndi thanthwe pamaso pao, kuti liwapatse madzi; potero uwaturutsire madzi m'thanthwe, ndi kumwetsa khamu la anthu ndi zoweta zao.

Werengani mutu wathunthu Numeri 20