Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 2:25-32 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

25. Mbendera ya cigono ca Dani izikhala kumpoto monga mwa makamu ao; ndi kalonga wa ana a Dani ndiye Ahiyezeri mwana wa Amisadai.

26. Ndi khamu lace, ndi owerengedwa ace, ndiwo zikwi makumi asanu ndi limodzi mphambu ziwiri kudza mazana asanu ndi awiri.

27. Ndipo iwo akumanga mahema ao poyandikizana naye ndiwo a pfuko la Aseri; ndi kalonga wa ana a Aseri ndiye Pagiyeli mwana wa Okirani.

28. Ndi khamu lace, ndi owerengedwa ace, ndiwo zikwi makumi anai mphambu cimodzi kudza mazana asanu.

29. Ndi pfuko la Nafitali: ndi kalonga wa ana a Nafitali ndiye Ahira mwana wa Enani.

30. Ndi khamu lace, ndi owerengedwa ace, ndiwo zikwi makumi asanu mphambu zitatu kudza mazana anai.

31. Owerengedwa onse a cigono ca Dani ndiwo zikwi makumi khumi mphambu makumi asanu kudza zisanu ndi ziwiri mphambu mazana asanu ndi Hmodzi. Iwo ndiwo aziyenda m'mbuyo paulendo, monga mwa mbendera zao.

32. Amenewo ndiwo anawerengedwa a ana a Israyeli monga mwa nyumba za makolo ao; owerengedwa onse a m'zigono, monga mwa makamu ao, ndiwo zikwi makumi khumi kasanu ndi kamodzi mphambu zitatu kudza mazana asanu ndi makumi asanu.

Werengani mutu wathunthu Numeri 2