Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 19:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nati,

2. Ili ndi lemba la cilamulo Yehova adalamuliraci, ndi kuti, Nena ndi ana a Israyeli kuti azikutengera ng'ombe ramsoti yofiira, yangwiro yopanda enema, yosamanga m'goli;

3. ndipo muipereke kwa Eleazara wansembe, naiturutse iye kunja kwa cigono, ndipo wina aiphe pamaso pace.

4. Ndipo Eleazara wansembe atengeko mwazi wace ndi cala cace, nawazeko mwazi wace kasanu ndi kawiri pakhomo pa cihema cokomanako.

5. Pamenepo atenthe ng'ombe yamsotiyo pamaso pace; atenthe cikopa cace ndi nyama yace, ndi mwazi wace, pamodzi ndi cipwidza cace.

6. Ndipo wansembe atenge mtengo wamkungudza, ndi hisope, ndi ubweya wofiira, naziponye pakati pa mota irikupsererapo ng'ombe yamsoti.

Werengani mutu wathunthu Numeri 19