Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 17:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

2. Nena ndi ana a Israyeli, nulandire kwa yense ndodo, banja liri onse la makolo ndodo imodzi, mafuko ao onse monga mwa mabanja a makolo ao azipereka ndodo, zikhale khumi ndi ziwiri; nulembe dzina la yense pa ndodo yace.

3. Ndipo ulembe dzina la Aroni pa ndodo ya Levi; pakuti pakhale ndodo imodzi pa mkuru yense wa nyumba za makolo ao.

4. Ndipo uziike m'cihema cokomanako, cakuno ca mboni, kumene ndikomana ndi inu.

Werengani mutu wathunthu Numeri 17