Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 12:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Miriamu ndi Aroni anatsutsana naye Mose cifukwa ca mkazi mtundu wace Mkusi amene adamtenga; popeza adatenga mkazi Mkusi.

2. Ndipo anati, Kodi Yehova wanena ndi Mose yekha? sananenanso ndi ife nanga? Ndipo Yehova anamva.

3. Koma munthuyu Mose ndiye wofatsa woposa anthu onse a pa dziko lapansi.

4. Ndipo Yehova anati kwa Mose, ndi Aroni, ndi Miriamu modzidzimutsa, Turukani inu atatu kudza ku cihema cokomanako. Pamenepo anaturuka atatuwo.

5. Ndipo Yehova anatsika mumtambo njo, naima pa khomo la cihema, naitana Aroni ndi Miriamu; naturuka onse awiri.

6. Ndipo anati, Tamvani tsono mau anga; pakakhala mneneri pakati pa inu, Ine Yehova ndidzizindikiritsa kwa iye m'masomphenya, ndinena naye m'kulota.

7. Satero mtumiki wanga Mose; ndiye wokhulupirika m'nyumba mwanga monse.

8. Ndimanena naye pakamwa ndi pakamwa, maonekera, osati mophiphiritsa; ndipo amapenyerera maonekedwe a Yehova; potero munalekeranji kuopa kutsutsana naye mtumiki wanga, Mose.

Werengani mutu wathunthu Numeri 12