Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 11:4-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Ndipo anthu osokonezeka ali pakati pao anagwidwa naco cilakolako; ndi ana a Israyeli omwe analiranso, nati, Adzatipatsa nyama ndani?

5. Tikumbukira nsomba tinazidya m'Aigupto cabe, mankaka, ndi mavwendi, ndi anyesi a mitundu itatu;

6. koma tsopano moyo wathu waphwa; tiribe kanthu pamaso pathu koma mana awa.

7. Ndipo mana ananga zipatso zampasa, ndi maonekedwe ace ngati maonekedwe a bedola.

8. Anthu amamka, nawaola, nawapera ndi mphero, kapena kuwasinja mumtondo, nawaphika m'mphika, nawaumba timitanda; ndi powalawa anali ngati timitanda tokazinga ndi mafuta.

9. Ndipo pakugwa mame pacigono usiku, mana anagwapo.

10. Ndipo Mose anamva anthu alikulira m'mabanja ao, yense pakhomo pa hema wace; ndipo Yehova anapsa mtima ndithu, ndipo kudamuipira Mose.

Werengani mutu wathunthu Numeri 11