14. Ndipo anayamba kuyenda a mbendera ya cigono ca ana a Yuda monga mwa magulu ao; woyang'anira gulu lace ndiye Nahesoni mwana wa Aminadabu.
15. Ndi pa gulu la pfuko la ana a Isakara panali Netaneli mwana wa Zuwara.
16. Ndi pa gulu la pfuko la ana a Zebuloni panali Eliyabu mwana wa Heloni.
17. Ndipo anagwetsa kacisi; ndi ana a Gerisoni, ndi ana a Merari, akunyamula kacisi, anamuka naye.
18. Ndi a mbendera ya cigono ca Rubeni, anayenda monga mwa magulu ao; ndipo pa gulu lace anayang'anira Elizuri mwana wa Sedeuri.
19. Ndi pa gulu la pfuko la ana a Simeoni anayang'anira Selumiyeli mwana wa Zurisadai.
20. Ndi pa gulu la pfuko la ana a Gadi anayang'anira Eliyasafe mwana wa Deyueli.
21. Pamenepo Akohati anayenda, ndi kunyamula zopatulika, ndi enawo anautsiratu kacisi asanafike iwowa.
22. Ndipo anayenda a mbendera ya cigono ca ana a Efraimu, monga mwa magulu ao; ndi pa gulu lace anayang'anira Elizama mwana wa Amihudi.
23. Ndi pa gulu la pfuko la ana a Manase anayang'anira Gamaliyeli mwana wa Pedazuri.
24. Ndi pa gulu la pfuko la ana a Benjamini anayang'anira Abidana mwana wa Gideoni.
25. Pamenepo anayenda a mbendera ya cigono ca ana a Dani, ndiwo a m'mbuyombuyo a zigono zonse, monga mwa magulu ao; ndi pa gulu lace anayang'anira Ahiyezeri mwana wa Amisadai.