Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 1:43-53 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

43. owerengedwa ao a pfuko la Nafitali, ndiwo zikwi makumi asanu mphambu zitatu kudza mazana anai.

44. Iwo ndiwo amene anawerengedwa, amene Mose anawerenga pamodzi ndi Aroni, ndi akalonga a Israyeli, ndiwo amuna khumi ndi awiri; yense kunenera nyumba ya kholo lace.

45. Potero owerengedwa onse a ana a Israyeli monga mwa nyumba za makolo ao, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akuturukira kunkhondo m'Israyeli;

46. inde owerengedwa onse ndiwo zikwi mazana asanu ndi limodzi mphambu zitatu kudza mazana asanu ndi makumi asanu.

47. Koma Alevi monga mwa pfuko la makolo ao sanawerengedwa mwa iwo.

48. Popeza Yehova adalankhula ndi Mose, ndi kuti,

49. Pfuko la Levi lokha usaliwerenge, kapena kuona kufikira kwao mwa ana a Israyeli;

50. koma iwe, uike Alevi asunge kacisi wa mboni, ndi zipangizo zace zonse, ndi zonse ali nazo; azinyamula kacisi, ndi zipangizo zace zonse; namtumikire, namange mahema ao pozungulira pa kacisi.

51. Ndipo akati amuke naye kacisiyo, Aleviamgwetse, ndipo akati ammange, Alevi amuimike; ndipo mlendo akayandikizako amuphe,

52. Ndipo ana a Israyeli amange mahema ao, yense ku cigono cace, ndi yense ku mbendera yace, monga mwa makamu ao.

53. Koma Alevi amange mahema ao pozungulira pa kacisi wa mboni, kuti mkwiyo ungagwere khamu la ana a Israyeli; ndipo Alevi azidikira kacisi wa mboni.

Werengani mutu wathunthu Numeri 1