28. A ana a Isakara, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akuturukira kunkhondo;
29. owerengedwa ao a pfuko la lsakara, ndiwo zikwi makumi asanu mphambu zinai kudza mazana anai.
30. A ana a Zebuloni, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akuturukira kunkhondo;
31. owerengedwa ao a pfuko la Zebuloni, ndiwo zikwi makumi asanu mphambu zisanu ndi ziwiri kudza mazana anai.
32. A ana a Yosefe, ndiwo a ana a Efraimu, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akuturukira kunkhondo;
33. owerengedwa ao a pfuko la Efraimu, ndiwo zikwi makumi anai mphambu mazana asanu.
34. A ana a Manase, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akuturukira kunkhondo;
35. owerengedwa ao a pfuko la Manase, ndiwo zikwi makumi atatu mphambu ziwiri kudza mazana awiri.
36. A ana a Benjamini, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akuturukira kunkhondo;
37. owerengedwa ao a pfuko la Benjamini, ndiwo zikwi makumi atatu mphambu zisanu kudza mazana anai.
38. A ana a Dani, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akuturukira kunkhondo;
39. owerengedwa ao a pfuko la Dani, ndiwo zikwi makumi asanu ndi limodzi mphambu ziwiri kudza mazana asanu ndi awiri.
40. A ana a Aseri, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akuturukira kunkhondo;
41. owerengedwa ao a pfuko la Aseri, ndiwo zikwi makumi anai mphambu cimodzi kudza mazana asanu.
42. A ana a Nafitali, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akuturukira kunkhondo;
43. owerengedwa ao a pfuko la Nafitali, ndiwo zikwi makumi asanu mphambu zitatu kudza mazana anai.
44. Iwo ndiwo amene anawerengedwa, amene Mose anawerenga pamodzi ndi Aroni, ndi akalonga a Israyeli, ndiwo amuna khumi ndi awiri; yense kunenera nyumba ya kholo lace.
45. Potero owerengedwa onse a ana a Israyeli monga mwa nyumba za makolo ao, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akuturukira kunkhondo m'Israyeli;
46. inde owerengedwa onse ndiwo zikwi mazana asanu ndi limodzi mphambu zitatu kudza mazana asanu ndi makumi asanu.
47. Koma Alevi monga mwa pfuko la makolo ao sanawerengedwa mwa iwo.