Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 1:13-33 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Wa Aseri, Pagiyeli mwana wa Okirani.

14. Wa Gadi, Eliyasafe mwana wa Deyueli.

15. Wa Nafitali, Ahira mwana wa Enani.

16. Iwo ndiwo oitanidwa a khamu, akalonga a mapfuko a makolo ao; ndiwo akuru a zikwizo za Israyeli.

17. Ndipo Mose ndi Aroni anatenga anthu awa, onenedwa maina ao;

18. nasonkhanitsa khamu lonse tsiku loyamba la mwezi waciwiri, ndipo iwo anawakumbira magwero ao kuchula mabanja ao, ndi nyumba za makolo ao, ndi kuwerenga maina kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu mmodzi mmodzi.

19. Monga Yehova anauza Mose, momwemo anawawerenga m'cipululu ca Sinai.

20. Ndipo ana a Rubeni, mwana woyamba wa Israyeli, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina mmodzi mmodzi, amuna onse kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akuturukira kunkhondo;

21. owerengedwa ao a pfuko la Rubeni, ndiwo zikwi makumi anai mphambu zisanu ndi cimodzi kudza mazana asanu.

22. A ana a Simeoni, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, owerengedwa ao, powerenga maina mmodzi mmodzi, amuna onse kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akuturukira kunkhondo;

23. owerengedwa ao a pfuko la Simeoni, ndiwo zikwi makumi asanu mphambu zisanu ndi zinai kudza mazana atatu.

24. A ana a Gadi, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akuturukira kunkhondo;

25. owerengedwa ao a pfuko la Gadi, ndiwo zikwi makumi anai mphambu zisanu kudza mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu.

26. A ana a Yuda, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makomi awiri ndi mphambu, onse akuturukira kunkhondo;

27. owerengedwa ao a pfuko la Yuda, ndiwo zikwi makumi asanu ndi awiri mphambu zinai kudza mazana asanu ndi limodzi.

28. A ana a Isakara, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akuturukira kunkhondo;

29. owerengedwa ao a pfuko la lsakara, ndiwo zikwi makumi asanu mphambu zinai kudza mazana anai.

30. A ana a Zebuloni, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akuturukira kunkhondo;

31. owerengedwa ao a pfuko la Zebuloni, ndiwo zikwi makumi asanu mphambu zisanu ndi ziwiri kudza mazana anai.

32. A ana a Yosefe, ndiwo a ana a Efraimu, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akuturukira kunkhondo;

33. owerengedwa ao a pfuko la Efraimu, ndiwo zikwi makumi anai mphambu mazana asanu.

Werengani mutu wathunthu Numeri 1