Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 1:1-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. NDIPO Yehova ananena ndi Mose m'cipululu ca Sinai, m'cihema cokomanako, tsiku loyamba la mwezi waciwiri, caka caciwiri ataturuka m'dziko la Aigupto, ndi kuti,

2. Werenga khamu lonse la ana a Israyeli, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba ya makolo ao ndi kuwerenga maina ao, amuna onse mmodzi mmodzi.

3. Iwe ndi Aroni muwawerenge monga mwa magulu ao, onse m'Israyeli akuturuka kunkhondo, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu,

4. Ndipo pamodzi ndi inu pakhale munthu mmodzi wa mapfuko onse; yense mkuru wa nyumba ya kholo lace.

5. Ndipo maina a amuna amene aime nanu ndi awa: wa Rubeni, Elizuri mwana wa Sedeuri.

6. Wa Simeoni, Selumiyeli mwana wa Zurisadai.

7. Wa Yuda, Nahesoni mwana wa Aminadabu.

8. Wa Isakara, Netaneli mwana wa Zuwara.

9. Wa Zebuloni, Eliyabu mwana wa Heloni.

10. Wa ana a Yosefe: wa Efraimu, Elisama mwana wa Amihudi; wa Manase, Gamaliyeli mwana wa Pedazuri.

11. Wa Benjamini, Abidana mwana wa Gideoni.

Werengani mutu wathunthu Numeri 1