Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Nehemiya 7:28-38 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

28. Amuna a ku Bete-Azimaveti, makumi anai kudza awiri.

29. Amuna a ku Kiriyati Yearimu, Kefiira, ndi Beeroti, mazana asanu ndi awiri mphambu makumi anai kudza atatu.

30. Amuna a ku Rama ndi Geba, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi awiri kudza mmodzi.

31. Amuna a ku Mikimasi, zana limodzi mphambu makumi awiri kudza awiri.

32. Amuna a ku Betele ndi Ai, zana limodzi mphambu makumi awiri kudza atatu.

33. Amuna a ku Nebo winayo, makumi asanu kudza awiri.

34. Ana a Elamu winayo, cikwi cimodzi mphambu mazana awiri ndi makumi asanu kudza anai.

35. Ana a Harimu, mazana atatu mphambu makumi awiri.

36. Ana a Yeriko, mazana atatu mphambu makumi anai kudza asanu.

37. Ana a Lodi, Hadidi, ndi Ono, mazana asanu ndi awiri mphambu makumi awiri kudza mmodzi.

38. Ana a Senaa, zikwi zitatu mphambu mazana asanu ndi anai kudza makumi atatu.

Werengani mutu wathunthu Nehemiya 7