19. Ana a Bigivai, zikwi ziwiri mphambu makumi asanu ndi limodzi kudza asanu ndi awiri.
20. Ana a Adini, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu kudza asanu.
21. Ana a Aberi, a Hezekiya, makumi asanu ndi anai kudza asanu ndi atatu.
22. Ana a Hasumu, mazana atatu mphambu makumi awiri kudza asanu ndi atatu.
23. Ana a Bezai, mazana atatu mphambu makumi awiri kudza anai.
24. Ana a Harifi, zana limodzi mphambu khumi ndi awiri.
25. Ana a Gibeoni, makumi asanu ndi anai kudza asanu.