17. Ana a Azigadi, zikwi ziwiri mphambu mazana atatu kudza makumi awiri ndi awiri.
18. Ana a Adonikamu, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu ndi limodzi, kudza asanu ndi awiri.
19. Ana a Bigivai, zikwi ziwiri mphambu makumi asanu ndi limodzi kudza asanu ndi awiri.
20. Ana a Adini, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu kudza asanu.
21. Ana a Aberi, a Hezekiya, makumi asanu ndi anai kudza asanu ndi atatu.
22. Ana a Hasumu, mazana atatu mphambu makumi awiri kudza asanu ndi atatu.