13. Ana a Zatu, mazana asanu ndi atatu mphambu makumi anai kudza asanu.
14. Ana a Zakai, mazana asanu ndi awiri mphambu makumi asanu ndi limodzi.
15. Ana a Binui, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi anai kudza asanu ndi atatu.
16. Ana a Betai, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi awiri kudza asanu ndi atatu.
17. Ana a Azigadi, zikwi ziwiri mphambu mazana atatu kudza makumi awiri ndi awiri.
18. Ana a Adonikamu, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu ndi limodzi, kudza asanu ndi awiri.
19. Ana a Bigivai, zikwi ziwiri mphambu makumi asanu ndi limodzi kudza asanu ndi awiri.
20. Ana a Adini, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu kudza asanu.
21. Ana a Aberi, a Hezekiya, makumi asanu ndi anai kudza asanu ndi atatu.
22. Ana a Hasumu, mazana atatu mphambu makumi awiri kudza asanu ndi atatu.
23. Ana a Bezai, mazana atatu mphambu makumi awiri kudza anai.