1. Kunali tsono, atamva Sanibalati, ndi Tobiya, ndi Gesemu M-arabu, ndi adani athu otsala, kuti ndidatha kumanga lingali, posatsalaponso popasuka; (ngakhale pajapo sindinaika zitseko pazipata);
2. anatumiza mau kwa ine Sanibalati ndi Gesemu, kuti, Tiyeni tikomane ku midzi ya ku cigwa ca Ono; koma analingirira za kundicitira coipa.
3. Ndipo ndinawatumizira mithenga, ndi kuti, Ndirikucita nchito yaikuru, sindikhoza kutsika; ndiidulirenji padera nchito poileka ine, ndi kukutsikirani?
4. Nanditumizira ine mau otere kanai; ndinawabwezeranso mau momwemo.