Cifukwa cace ndinawaika potera m'kati mwa linga, popenyeka; inde ndinaika anthu monga mwa mabanja ao, akhale nao malupanga ao, nthungo zao, ndi mauta ao.