Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Nehemiya 3:22-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

22. Ndi potsatizana naye anakonza ansembe okhala kucidikha.

23. Potsatizana nao anakonza Benjamini ndi Hasubi pandunji pa nyumba pao, Potsatizana nao anakonza Azariya mwana wa Maseya mwana wa Ananiya pafupi pa nyumba yace.

24. Potsatizana naye Binui mwana wa Henadadi anakonza gawo lina, kuyambira ku nyumba ya Azariya kufikira popindirira kufikira kungondya.

25. Palali mwana wa Uzai anakonza pandunji popindirira, ndi nsanja yosomphoka pa nyumba ya mfumu ya kumtunda, imene iri ku bwalo la kaidi. Potsatizana naye anakonza Pedaya mwana wa Parosi.

26. Koma Anetini okhala m'Ofeli anakonza kufikira ku malo a pandunji pa cipata ca kumadzi kum'mawa, ndi nsanja yosomphokayo,

27. Potsatizana nao Atekoa anakonza gawo lina, pandunji pa nsanja yaikuru yosomphoka ndi ku linga la Ofeli.

28. Kumtunda kwa cipata ca akavalo anakonza ansembe, yense pandunji pa nyumba yace.

Werengani mutu wathunthu Nehemiya 3