Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Nehemiya 13:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Tsiku lomwelo anawerenga m'buku la Mose m'makutu a anthu, napeza m'menemo kuti Aamoni ndi Amoabu asalowe mu msonkhano wa Mulungu ku nthawi yonse;

2. popeza sanawacingamira ana a Israyeli ndi cakudya ndi madzi, koma anawalemberera Balamu awatemberere; koma Mulungu wathu anasanduliza tembererolo likhale mdalitso.

3. Ndipo kunali, atamva cilamuloco, anasiyanitsa pa Israyeli anthu osokonezeka onse.

4. Cinkana ici, Eliasibu wansembe, woikidwa asunge zipinda za nyumba ya Mulungu wathu, anacita cibale ndi Tobiya,

Werengani mutu wathunthu Nehemiya 13