10. Ndi Yesuwa anabala Yoyakimu, ndi Yoyakimu anabala Eliasibi ndi Eliasibi anabala Yoyada,
11. ndi Yoyada anabala Yonatani, ndi Yonatani, anabala Yaduwa.
12. Ndi m'masiku a Yoyakimu ansembe akulu a nyumba za makolo ndiwo: wa Seraya, Meraya; wa Yeremiya, Hananiya;
13. wa Ezara, Mesulamu; wa Amariya, Yehohanana;
14. wa Maluki, Yonatani; wa Sebaniya, Yosefe;
15. wa Harimu, Adina; wa Merayoti, Helikai;
16. wa Ido, Zekariya; wa Ginetoni, Mesulamu;
17. wa Abiya, Zikiri; wa Minyamini, wa Moadiya, Pilitai;
18. wa Biliga, Samura; wa Semaya, Yehonatani;
19. ndi wa Yoyaribi, Matani; wa Yedaya, Uzi;
20. wa Salai, Kalai; wa Amoki, Eberi;
21. wa Hilikiya, Hasabiya; wa Yedaya, Netaneli.
22. M'masiku a Ehasibi, Yoyada, Yohanana, ndi Yoduwa, Alevi analembedwa akuru a nyumba za makolo; ansembe omwe, mpaka ufumu wa Dariyo wa ku Perisiya.
23. Ana a Levi, akuru a nyumba za makolo, analembedwa m'buku la macitidwe, mpaka masiku a Yohanana mwana wa Eliasibu.