Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Nehemiya 11:24-36 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

24. Ndi Petatiya mwana wa Mesezabele, wa ana a Zera, mwana wa Yuda, anatumikira mfumu pa mirandu yonse ya anthuwo.

25. Ndi ana ena a Yuda anakhala m'midzi ya ku minda yao, m'Kiriyati Ariba ndi miraga yace, ndi m'Diboni ndi miraga yace, ndi m'Yekabizeeli ndi midzi yace,

26. ndi m'Yesuwa, ndi m'Molada, ndi Betepeleti,

27. ndi m'Hazarisuala, ndi m'Beereseba ndi miraga yace,

28. ndi m'Zikilaga, ndi m'Mekona ndi miraga yace,

29. ndi m'Enirimoni, ndi m'Zora, ndi m'Yarimuti,

30. Zanowa, Adulamu ndi midzi yao, Lakisi ndi minda yace, Azeka ndi miraga yace. Ndipo anamanga misasa kuyambira ku Beereseba mpaka cigwa ca Hinomu.

31. Ana a Benjamini omwe, kuyambira ku Geba pa Mikimasi, ndi Aiya, ndi pa Beteli ndi miraga yace,

32. pa Anatoti, Nobi, Ananiya,

33. Hazori, Rama, Gitaimu,

34. Hadidi, Zeboimu, Nebalati,

35. Lodi, ndi Ono, cigwa ca amisiri.

36. Ndi magawo a Levi anakhala ena ku Yuda, ndi ena ku Benjamini.

Werengani mutu wathunthu Nehemiya 11