Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Nahumu 1:5-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Mapiri agwedezeka cifukwa ca Iye, ndi zitunda zisungunuka; ndi dziko lapansi likwezeka pamaso pace, ndi maiko ndi onse okhala m'mwemo.

6. Adzaima ndani pa kulunda kwace? ndipo adzakhalitsa ndani pa mkwiyo wace wotentha? ukali wace utsanulidwa ngati moto, ndi matanthwe asweka ndi Iye.

7. Yehova ali wabwino, ndiye polimbikirapo tsiku la msauko; ndipo adziwa iwo omkhulupirira Iye.

8. Koma ndi cigumula cosefukira adzatha konse malo ace, nadzapitikitsira adani ace kumdima.

9. Mulingaliranji cotsutsana ndi Yehova? Iye adzatha psiti; nsautso siidzauka kawiri.

10. Pakuti cinkana akunga minga yoyangayanga, naledzera naco coledzeretsa cao, adzathedwa konse ngati ciputu couma.

Werengani mutu wathunthu Nahumu 1