Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Nahumu 1:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. KATUNDU wa Nineve. Buku la masomphenya a Nahumu wa ku Elikosi.

2. Yehova ndiye Mulungu wansanje, nabwezera cilango; Yehova ndiye wobwezera cilango, ndi waukali ndithu; Yehova ndiye wobwezera cilango oyambana naye, nasungira mkwiyo pa adani ace.

3. Yehova ndiye wolekerera mkwiyo, koma wa mphamvu yaikuru; ndi wosamasula ndithu woparamula; njira ya Yehova iri m'kabvumvulu ndi mumkuntho; ndipo mitambo ndiyo pfumbi la mapazi ace.

4. Adzudzula nyanja, naiphwetsa, naumitsa mitsinje yonse; Basana ndi Karimeli afota, ndi duwa la ku Lebano linyala.

5. Mapiri agwedezeka cifukwa ca Iye, ndi zitunda zisungunuka; ndi dziko lapansi likwezeka pamaso pace, ndi maiko ndi onse okhala m'mwemo.

6. Adzaima ndani pa kulunda kwace? ndipo adzakhalitsa ndani pa mkwiyo wace wotentha? ukali wace utsanulidwa ngati moto, ndi matanthwe asweka ndi Iye.

7. Yehova ali wabwino, ndiye polimbikirapo tsiku la msauko; ndipo adziwa iwo omkhulupirira Iye.

8. Koma ndi cigumula cosefukira adzatha konse malo ace, nadzapitikitsira adani ace kumdima.

9. Mulingaliranji cotsutsana ndi Yehova? Iye adzatha psiti; nsautso siidzauka kawiri.

Werengani mutu wathunthu Nahumu 1