Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Mlaliki 8:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndani akunga wanzeru? Ndani adziwa tanthauzo la mau? Nzeru ya munthu iwalitsa nkhope yace, kuduwa kwa nkhope yace ndi kusanduka.

2. Nditi, Sunga mau a mfumu, makamaka m'kulumbira Mulungu.

3. Usakangaze kumcokera; usaumirire kanthu koipa; pakuti iyeyo amacita comwe cimkonda.

4. Pakuti mau a mfumu ali ndi mphamvu; ndipo ndani anganene kwa iye, Kodi ucita ciani?

5. Wosunga cilamulo sadzadziwa kanthu koipa; ndipo mtima wa munthu wanzeru udziwa nyengo ndi maweruzo;

6. pakuti kanthu kali konse kali ndi nthawi yace ndi ciweruzo cace; popeza zoipa za munthu zimcurukira;

7. pakuti sadziwa cimene cidzakhala; pakuti ndani angamuuze nthawi yakuti cidzacitidwa?

8. Kulibe munthu ali ndi mphamvu yolamulira mzimu ndi yakutsekereza mzimu; ngakhale mphamvu tsiku la imfa; munkhondo umo mulibe kumasuka; udio sudzapulumutsa akuzolowerana nao.

9. Zonsezi ndaziona ndi kuyang'anitsa mtima wanga nchito zonse zicitidwa pansi pano; nthawi yakuti wina apweteka mnzace pomlamulira.

Werengani mutu wathunthu Mlaliki 8