Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Mlaliki 7:1-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Mbiri yabwino iposa zonunkhira zabwino; ndi tsiku lakumwalira liposa tsiku lakubadwa.

2. Kunka ku nyumba ya maliro kupambana kunka ku nyumba ya madyerero; pakuti kujako ndi matsiriziro a anthu onse; ndipo omwe ali ndi moyo adzakumbukirapo.

3. Cisoni ciposa kuseka; pakuti nkhope yakugwa ikonza mtima.

4. Mtima wa anzeru uli m'nyumba ya maliro; koma mtima wa zitsiru uli m'nyumba ya kuseka.

5. Kumva cidzudzulo ca anzeru kupambana kumva nyimbo ya zitsiru.

6. Pakuti kuseka kwa citsiru kunga minga irikutetheka pansi pa mphika; icinso ndi cabe.

7. Indetu nsautso iyarutsa wanzeru; ndi mtulo uipitsa mtima.

8. Citsiriziro ca kanthu ciposa ciyambi cace; wofatsa mtima apambana wodzikuza mtima.

9. Usakangaze mumtima mwako kukwiya; pakuti mkwiyo ugona m'cifuwa ca zitsiru.

10. Usanene, Kodi bwanji masiku akale anapambana ano? Pakuti sulikufunsa mwanzeru pamenepo.

11. Nzeru iri yabwino pamodzi ndi colowa; akuona dzuwa apindula nayo.

12. Pakuti nzeru icinjiriza monga ndalama zicinjiriza; koma kudziwa kupambana, cifukwa nzeru isunga moyo wa eni ace.

13. Tapenya nchito ya Mulungu; pakuti ndani akhoza kulungamitsa comwe iye anacikhotetsa?

14. Tsiku la mwai kondwera, koma tsiku la tsoka lingirira; Mulungu waika ici pambali pa cinzace, kuti anthu asapeze kanthu ka m'tsogolo mwao.

Werengani mutu wathunthu Mlaliki 7