Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Mlaliki 4:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndinabweranso tsono ndi kupenyera nsautso zonse zimacitidwa kunja kuno; ndipo taona, misozi ya otsenderezedwa, koma analibe wakuwatonthoza; ndipo akuwatsendereza anali ndi mphamvu koma iwowa analibe wakuwatonthoza.

2. Ndipo ndinatama akufa atatha kufa kupambana amoyo omwe alipobe;

3. inde yemwe sanabadwe konse aposa onse awiriwo popeza sanaone nchito yoipa yocitidwa kunja kuno.

4. Ndiponso ndinapenyera mabvuto onse ndi nchito zonse zompindulira bwino, kuti cifukwa ca zimenezi anansi ace acitira munthu nsanje. Icinso ndi cabe ndi kungosautsa mtima.

5. Citsiru cimanga manja ace, nicidya nyama yace yace.

6. Dzanja limodzi lodzala pali mtendere liposa manja awiri oti tho pali bvuto ndi kungosautsa mtima.

Werengani mutu wathunthu Mlaliki 4