Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Mlaliki 3:5-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. mphindi yakutaya miyala ndi mphindi yakukundika miyala; mphindi yakufungatirana ndi mphindi yakuleka kufungatirana;

6. mphindi yakufunafuna ndi mphindi yakumwazika; mphindi yakusunga ndi mphindi yakutaya;

7. mphindi yakung'amba ndi mphindi yakusoka; mphindi yakutonthola ndi mphindi yakulankhula;

8. mphindi yakukonda ndi mphindi yakudana; mphindi ya nkhondo ndi mphindi ya mtendere.

9. Wogwira nchito aona phindu lanji m'comsautsaco?

10. Ndaona bvuto limene Mulungu wapatsa ana a anthu kuti abvutidwe nalo.

11. Cinthu ciri conse anacikongoletsa pa mphindi yace; ndipo waika zamuyaya m'mitima yao ndipo palibe munthu angalondetse nchito Mulungu wazipanga ciyambire mpaka citsiriziro.

12. Ndidziwa kuti iwo alibe ubwino, koma kukondwa ndi kucita zabwino pokhala ndi moyo.

13. Ndiponso kuti munthu yense adye namwe naone zabwino m'nchito zace zonse; ndiwo mtulo wa Mulungu.

14. Ndidziwa kuti zonse Mulungu azicita zidzakhala kufikira nthawi zonse; sungaonjezepo kanthu, ngakhale kucotsapo; Mulungu nazicita kuti anthu akaope pamaso pace.

15. Cocomwe cinaoneka, cirikuonekabe; ndi comwe cidzaoneka cinacitidwa kale; Mulungu anasanthula zocitidwa kale.

Werengani mutu wathunthu Mlaliki 3