1. Kanthu kali konse kali ndi nthawi yace ndi cofuna ciri conse ca pansi pa thambo ciri ndi mphindi yace;
2. mphindi yakubadwa ndi mphindi yakumwalira; mphindi yakubzyala ndi mphindi yakuzula zobzyalazo;
3. mphindi yakupha ndi mphindi yakuciza; mphindi yakupasula ndi mphindi yakumanga;
4. mphindi yakugwa misozi ndi mphindi yakuseka; mphindi yakulira ndi mphindi yakubvina;
5. mphindi yakutaya miyala ndi mphindi yakukundika miyala; mphindi yakufungatirana ndi mphindi yakuleka kufungatirana;