Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Mlaliki 12:9-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Ndiponso pokhala wanzeru Mlalikiyo anaphunzitsabe anthu nzeru; inde, anachera makutu nafunafuna nalongosolamiyambiyambiri.

10. Mlalikiyo anasanthula akapeze mau okondweretsa, ndi zolemba zoongoka ngakhale mau oona.

11. Mau a anzeru akunga zisonga, omwe akundika mau amene mbusa mmodzi awapatsa mau ao akunga misomali yokhomedwa zolimba.

12. Pamodzi ndi izi, mwananga, tacenjezedwa; pakuti saleka kulemba mabuku ambiri; ndipo kuphunzira kwambiri kutopetsa thupi.

13. Mau atha; zonse zamveka zatha; opa Mulungu, musunge malamulo ace; pakuti coyenera anthu onse ndi ici.

14. Pakuti Mulungu adzanena mlandu wa zocita zonse, ndi zobisika zonse, ngakhale zabwino ngakhale zoipa.

Werengani mutu wathunthu Mlaliki 12