Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Mlaliki 10:5-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Pali coipa ndaciona pansi pano, ngati kulakwa koyambira ndi mkuru;

6. utsiru ukhazikika pamwamba penipeni, ndipo olemera angokhala mwamanyazi.

7. Ndaona akapolo atakwera pa akavalo, ndi mafumu, alikuyenda pansi ngati akapolo.

8. Wokumba mbuna adzagwamo; ndipo woboola mpanda njoka idzamluma.

9. Wosendeza miyala adzaphwetekedwa nayo; wowaza nkhuni nadzitema.

10. Citsulo cikakhala cosathwa, ndipo ukaleka kunola, uzipambana kulimbikira; koma nzeru ipindulira pocenjeza.

11. Njoka ikaluma isanalodzedwe, watsenga saona mphotho.

12. Mau a m'kamwa mwa munthu wanzeru nga cisomo; koma milomo ya citsiru idzacimeza.

13. Ciyambi ca mau a m'kamwa mwace ndi utsiru; ndipo cimariziro ca m'kamwa mwace ndi misala yoipa,

14. Citsiru cicurukitsanso mau; koma munthu sadziwa cimene cidzaoneka; ndipo ndani angamuuze comwe cidzakhala m'tsogolo mwace?

15. Nchito ya zitsiru izitopetsa zonsezo, pakuti sicidziwa kunka kumudzi.

16. Tsoka kwa dzikowe, pamene mfumu yako ndiye mwana, ndipo akalonga ako adyera mamawa!

Werengani mutu wathunthu Mlaliki 10