Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Mlaliki 10:5-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Pali coipa ndaciona pansi pano, ngati kulakwa koyambira ndi mkuru;

6. utsiru ukhazikika pamwamba penipeni, ndipo olemera angokhala mwamanyazi.

7. Ndaona akapolo atakwera pa akavalo, ndi mafumu, alikuyenda pansi ngati akapolo.

8. Wokumba mbuna adzagwamo; ndipo woboola mpanda njoka idzamluma.

9. Wosendeza miyala adzaphwetekedwa nayo; wowaza nkhuni nadzitema.

10. Citsulo cikakhala cosathwa, ndipo ukaleka kunola, uzipambana kulimbikira; koma nzeru ipindulira pocenjeza.

11. Njoka ikaluma isanalodzedwe, watsenga saona mphotho.

12. Mau a m'kamwa mwa munthu wanzeru nga cisomo; koma milomo ya citsiru idzacimeza.

13. Ciyambi ca mau a m'kamwa mwace ndi utsiru; ndipo cimariziro ca m'kamwa mwace ndi misala yoipa,

14. Citsiru cicurukitsanso mau; koma munthu sadziwa cimene cidzaoneka; ndipo ndani angamuuze comwe cidzakhala m'tsogolo mwace?

Werengani mutu wathunthu Mlaliki 10