8. Mau onse a m'kamwa mwanga alungama;Mwa iwo mulibe zokhota ndi zopotoka.
9. Onsewo amveka ndi iye amene azindikira;Alungama kwa akupeza nzeru.
10. Landirani mwambo wanga, si siliva ai;Ndi nzeru kopambana ndi golidi wosankhika.
11. Pakuti nzeru iposa ngale,Ndi zonse tizifunitsa sizilingana nayo,
12. Ine Nzeru ndikhala m'kucenjera, ngati m'nyumba yanga;Ndimapeza kudziwa ndi zolingalira.
13. Kuopa Yehova ndiko kuda zoipa;Kunyada, ndi kudzikuza, ndi njira yoipa, ndi m'kamwa mokhota, ndizida.
14. Ndine mwini uphungu ndi kudziwitsa;Ndine luntha; ndiri ndi mphamvu.
15. Mwa ine mafumu alamulira;Akazembe naweruza molungama.
16. Mwa ine akalonga ayang'anira,Ndi akuru, ngakhale oweruza onse a m'dziko,